Rute 4:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Boazi anakwera kumka kucipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Boazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, pambuka, khala pansi apa; napambuka iye, nakhala pansi.

2. Ndipo anatenga amuna khumi a akulu a mudzi, nati, Mukhale pansi apa. Nakhala pansi iwo.

3. Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Moabu ati agulitse kadziko kala kadali ka mbale wathu Elimeleki;

4. ndipo ndati ndikuululira ici, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso pa akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola.

Rute 4