Rute 3:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nubvundukule ku mapazi ace, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kucita iwe.

5. Ndipo ananena naye, Zonse muzinena ndidzacita.

6. Pamenepo anatsikira popunthirapo, nacita zonse monga umo mpongozi wace adamuuza.

7. Ndipo atatha Boazi kudya ndi kumwa, nusekerera mtima wace, anakagona kuthungo kwa mulu wa tirigu; nadza iye kacetecete, nabvuodukula ku mapazi ace, nagona.

8. Ndipo kunali, pakati pa usiku munthuyo anadzidzimuka, natembenuka; ndipo taona pa mapazi ace pagona mkazi.

9. Nati iye, Ndiwe yani? Nayankha iye, Ndine Rute mdzakazi wanu; mupfunde mdzakazi wanu copfunda canu, pakuti inu ndinu wondiombolera colowa.

10. Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Cokoma cako wacicita potsiriza pano, ciposa cakuyamba cija, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale acuma.

Rute 3