4. Nadzitengera iwo akazi a ku Moabu; wina dzina lace ndiye Olipa, mnzace dzina lace ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi.
5. Koma Maloni ndi Kilioni anamwalira onse awiri; motero ana ace amuna awiri ndi mwamuna wace anamsiya mkaziyo.
6. Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ace kuti abwerere kucoka m'dziko la Moabu; pakuti adamva m'dziko la Moabu kuti Yehova adasamalira anthu ace ndi kuwapatsa cakudya.
7. Naturuka iye kumene anakhalako ndi apongozi ace awiri pamodzi naye; namka ulendo wao kubwererakudzikola Yuda.
8. Ndipo Naomi anati kwa apongozi ace awiri, Mukani, bwererani yense wa inu ku nyumba ya amai wace; Yehova akucitireni zokoma, monga umo munacitira akufa aja ndi ine.
9. Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wace. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi.