Koma m'mudzimo munali nsanja yolimba nathawira kumeneko amuna ndi akazi onse, ndi eni ace onse a mudziwo, nadzitsekereza m'mwemo, nakwera patsindwi pa nsanja.