Oweruza 9:39-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Ndipo Gaala anaturuka pamaso pao pa eni ace a ku Sekemu, nalimbana ndi Abimeleki.

40. Koma Abimeleki anampitikitsa, nathawa iye pamaso pace; nagwa olasidwa ambiri mpaka polowera pa cipata.

41. Ndipo Abimeleki anakhala ku Aruma; ndi Zebuli anafngitsa Gaala ndi abale ace kuti asakhale m'Sekemu.

42. Ndipo kunali m'mawa mwace, kuti anthu anaturuka kumka kuminda; ndipo anauza Abimeleki.

43. Pamenepo anatenga anthu, nawagawa magulu atatu, nalalira m'minda; napenya, ndipo taonani, anthu alimkuturuka m'mudzi; nawaukira iye nawakantha.

44. Ndi Abimeleki ndi magulu okhala naye anathamanga naima polowera pa cipata ca mudzi; ndi magulu awiriwo anagwera onse okhala m'munda, nawakantha.

Oweruza 9