9. Ndipo pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israyeli mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyeli mwana wa'Kenazi, mng'ono wace wa Kalebe.
10. Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israyeli, naturuka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesapotamiya m'dzanja lace; ndi dzanja lace linamlaka Kusani-Risataimu.
11. Pamenepo dziko linapumula zaka makumi anai; ndi Otiniveli mwana wa Kenazi anafa.
12. Koma ana a Israyeli anaonjezanso kucita coipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Moabu pa Israyeli, popeza anacita coipa pamaso pa Yehova.
13. Ndipo anadzisonkanitsira ana a Amoni ndi a Amaleki, namuka nakantha Israyeli, nalanda mudzi wa m'migwalangwa nakhalamo.
14. Ndipo ana a Israyeli anatumildra Egiloni mfumu ya Moabu zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu.