4. Amenewo anakhala coyesera Israyeli kuti Yehova adziwe ngati adzamvere malamulo ace, amene analamulira makolo ao mwa dzanja la Mose.
5. Ndipo ana a Israyeli anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi;
6. nakwatira ana akazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana amuna a iwowa natumikira milungu yao.
7. Ndipo ana a Israyeli anacita coipa pamaso pa Yehova, naiwala Yehova Mulungu wao, natumikira Abaala ndi zifanizo.
8. Pamenepo mkwiyo wa Mulungu unayakira Israyeli ndipo anawagulitsa m'dzanja la KusaniRisataimu, mfumu ya Mesopotamiya; ndi ana a Israyeli anatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu.
9. Ndipo pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israyeli mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyeli mwana wa'Kenazi, mng'ono wace wa Kalebe.
10. Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israyeli, naturuka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesapotamiya m'dzanja lace; ndi dzanja lace linamlaka Kusani-Risataimu.
11. Pamenepo dziko linapumula zaka makumi anai; ndi Otiniveli mwana wa Kenazi anafa.
12. Koma ana a Israyeli anaonjezanso kucita coipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Moabu pa Israyeli, popeza anacita coipa pamaso pa Yehova.