1. Ndipo iyo ndiyo mitundu ya anthu anaisiyapo Yehova kuyesa nayo Israyeli, ndiwo onse amene sanadziwa nkhondo zonse za Kanani;
2. cifukwa cace ndico cokha cakuti adziwitse mibadwo ya ana a Israyeli ndi kuwaphunzitsa nkhondo, ngakhale iwo okha okha osaidziwa konse kale;
3. anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m'phiri la Lebano, kuyambira phiri la Baalaherimoni mpaka polowera ku Hamati.
4. Amenewo anakhala coyesera Israyeli kuti Yehova adziwe ngati adzamvere malamulo ace, amene analamulira makolo ao mwa dzanja la Mose.
5. Ndipo ana a Israyeli anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi;
6. nakwatira ana akazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana amuna a iwowa natumikira milungu yao.
7. Ndipo ana a Israyeli anacita coipa pamaso pa Yehova, naiwala Yehova Mulungu wao, natumikira Abaala ndi zifanizo.