Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m'mbuyo, naposa makolo ao ndi kucita moipitsa, ndi kutsata milungu yina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleka kanthu ka macitidwe ao kapena ka njira yao yacheni.