Ndipo ana a Dani anadziimitsira fane losemalo; ndi Yonatani mwana wa Gerisomu mwana wa Manase, iye ndi ana ace amuna anali ansembe a pfuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko.