Oweruza 10:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Nafa Yairi, naikidwa m'Kamoni.

6. Ndipo ana Israyeli a anaonjeza kucita coipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala, ndi Aastaroti, ndi milungu ya Aramu, ndi milungu ya Sidoni, ndi milungu ya Moabu, ndi milungu ya ana a Amoni, ndi milungu ya Afilisti; ndipo anamleka Yehova osamtumikira.

7. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli, nawagulitsa m'dzanja la Aftlisti, ndi m'dzanja la ana a Amoni.

8. Ndipo anaphwanya napsinja ana a Israyeli caka ciija, natero ndi ana onse a Israyeli okhala tsidya lija la Yordano m'dziko la Aamori, ndilo Gileadi, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu.

9. Ndipo ana a Amoni anaoloka Yordano kuthiranso nkhondo Yuda ndi Benjamini, ndi nyumba ya Efraimu; napsinjika kwambiri Israyeli.

10. Ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova ndi kuti, Takucimwirani, popeza tasiya Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.

11. Ndipo Yehova anati kwa ana a Israyeli, Kodi sindinakupulumutsani kwa Aaigupto ndi kwa Aamori, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Aftlisti?

12. Asidoni omwe, ndi Aamaleki, ndi Amidyani anakupsinjani. Pamenepo munapfuula kwa Ine, ndipo ndinakupulumutsani m'dzanja lao.

Oweruza 10