Oweruza 10:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israyeli Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye m'Sanriri ku mapiri a Efraimu.

2. Ndipo anaweruza Israyeli zaka makumi awiri ndi zitatu, nafa, naikidwa m'Samiri.

3. Atafa iye, anauka Yairi Mgileadi, naweruza Israyeli zaka makumi awiri mphambu ziwiri.

Oweruza 10