Oweruza 1:23-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo iwo a m'nyumba ya Yosefe anatumiza ozonda ku Beteli. Koma kale dzina la mudziwo ndilo Luzi.

24. Ndipo alonda anaona munthu alikuturuka m'mudzi, nanena naye, Utionetsetu nolowera m'mudzi, ndipo tidzakucitira cifundo.

25. Nawaonetsa polowera m'mudzi iye, naukantha mudzi iwowa ndi lupanga lakuthwa; koma analola munthuyo ndi banja lace lonse amuke.

Oweruza 1