Nyimbo 2:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza,Alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda.

9. Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala:Taona, aima patseri pa khoma pathu,Apenyera pazenera, Nasuzumira pamade.

10. Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine,Tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye.

11. Pakuti, taona, cisanu catha,Mvula yapita yaleka;

12. Maluwa aoneka pansi;Nthawi yoyimba mbalame yafika,Mau a njiwa namveka m'dziko lathu;

13. Mkuyu uchetsa nkhuyu zace zosakhwima,Mipesa niphuka,Inunkhira bwino.Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.

Nyimbo 2