Numeri 8:24-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ici ndi ca Alevi: kuyambira ali wa zaka makumi awiri ndi zisanu ndi mphambu azilowa kutumikira utumikiwu mu nchito ya cihema cokomanako;

25. ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osacitanso nchitoyi;

26. koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'cihema cokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira nchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.

Numeri 8