Numeri 7:66-69 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

66. Tsiku lakhumi kalonga wa ana a Dani, ndiye Ahiyezeri mwana wa Amisadai:

67. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;

68. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

69. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

Numeri 7