Numeri 7:44-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

44. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

45. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

46. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

47. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Eliyasafe mwana wa Deyueli.

48. Tsiku lacisanu ndi ciwiri kalonga wa ana a Efraimu Elisama mwana wa Amihudi:

49. copereka cace mbizi Imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

50. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

51. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

52. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

53. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa za mphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Elisama mwana wa Amihudi.

Numeri 7