Numeri 7:43-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

43. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu; mbale yowazira Imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

44. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

45. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

46. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

Numeri 7