Numeri 7:24-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Tsiku lacitatu kalonga wa ana a Zebuloni, ndiye Eliyabu mwana wa Heloni:

25. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

26. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

27. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

28. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

29. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Eliyabu mwana wa Heloni.

30. Tsiku lacinai Elizuri, mwana wa Sedeuri, kalonga wa ana a Rubeni:

Numeri 7