14. Mupereke midzi itatu tsidya lino la Yordano, ndi midzi itatu mupereke m'dziko la Kanani, ndiyo yopulumukirako.
15. Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israyeli, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti ali yense adamupha munthu osati dala athawireko.
16. Koma akamkantha ndi cipangizo cacitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
17. Kapena akamkantha m'dzanja muli mwala, wakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
18. Kapena akamkantha m'dzanja muli cipangizo camtengo, cakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
19. Wolipsa mwazi mwini wace aphe wakupha munthuyo; pakumkumika amuphe,
20. Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa;
21. kapena kumpanda ndi dzanja lace momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo pomkumika.