Numeri 35:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Moabu, pa Yordano, ku Yeriko, ndi kuti,

2. Uza ana a Israyeli, kuti apatseko Alevi colowa cao cao, midzi yokhalamo; muwapatsenso Alevi mabusa akuzungulira midzi.

3. Ndipo midzi ndiyo yokhalamo iwowa; ndi mabusa akhale a ng'ombe zao, ndi zoweta zao, inde nyama zao zonse.

4. Ndipo mabusa a midziyo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono cikwi cimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.

5. Ndipo muyese kunja kwa mudzi, mbali ya kum'mawa mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumwela mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumadzulo mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumpoto mikono zikwi ziwiri; ndi mudziwo pakati; ndiwo mabusa a kumidzi.

Numeri 35