12. ndi malire adzatsika ku Yordano, ndi kuturuka kwace kudzakhala ku Nyanja ya Mcere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ace polizinga.
13. Ndipo Mose anauza ana a Israyeli, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kucita maere, limene Yehova analamulira awapatse mapfuko asanu ndi anai ndi hafu;
14. popeza pfuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi pfuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi pfuko la hafu la Manase lalandira colowa cao;
15. mapfuko awiriwa ndi hafu adalandira colowa cao tsidya lija la Yordano ku Yeriko, kum'mawa, koturukira dzuwa.
16. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
17. Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale colowa canu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni.