51. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutaoloka Yordano kulowa m'dziko la Kanani,
52. mupitikitse onse okhala m'dzikopamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;
53. ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanu lanu.
54. Ndipo mulandire dzikoli ndi kucita maere monga mwa mabanja anu; colowa cao cicurukire ocurukawo, colowa cao cicepere ocepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwace; mulandire colowa canu monga mwa mapfuko a makolo anu.
55. Koma mukapanda kupitikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakubvutani m'dziko limene mukhalamo.