2. Ndipo Mose analembera maturukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa maturukidwe ao.
3. Ndipo anacokera ku Ramese mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi woyamba; atacita Paskha m'mawa mwace ana a Israyeli, anaturuka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aaigupto onse,
4. pamene Aaigupto ailalikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao.
5. Ndipo ana a Israyeli macokera ku Ramese, nayenda namanga ku Sukoti.
6. Nacokera ku Sukoti, nayenda namanga m'Etamu, ndiko ku malekezero a cipululu.
7. Ndipo anacokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwace kwa Baala Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli.
8. Ndipo anacokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'cipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'cipululu ca Etamu, namanga m'Mara.