Numeri 30:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo ngati anawinda m'nyumba ya mwamuna wace, kapena anamanga moyo wace ndi codziletsa ndi kulumbirapo,

11. ndipo mwanuna wace anamva, koma anakhala naye cete osamletsa, pamenepo zowinda zace zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wace zidzakhazikika.

12. Koma ngati mwamuna wace anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zoturuka m'milomo yace kunena za zowinda zace, kapena za codziletsa ca moyo wace sizidzakhazikika; mwamuna wace anazifafaniza; ndipo Yehova adzamkhululukira Iye.

13. Cowinda ciri conse, ndi columbira ciri conse codziletsa cakucepetsa naco moyo, mwamuna wace acikhazikira, kapena mwamuna wace acifafaniza.

14. Koma mwamuna wace akakhala naye cete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zace zonse, kapena zodziletsa zace zonse, ziri pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye cete tsikuli anazimva iye.

Numeri 30