Numeri 28:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi, pali paskha wa Yehova.

17. Ndipo tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi uwu pali madyerero; masiku asanu ndi awiri azidya mkate wopanda cotupitsa.

18. Tsiku loyamba pali kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena;

19. koma mubwere nayo nsembe yamoto, nsembe yopsereza ya Yehova; ng'ombe ziwiri zamphongo, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi; akhale kwa inu opanda cirema;

20. ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta; mupereke atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, ndi awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo;

21. upereke limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi; uzitero ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;

22. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo, yakutetezera inu.

Numeri 28