3. Atate wathu adamwalira m'cipululu, ndipo sanakhala iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zace zace; ndipo analibe ana amuna.
4. Licotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lace, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathu lathu pakati pa abale a atate wathu.
5. Ndipo Mose anapita nao mlandu wao pamaso pa Yehova.
6. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
7. Ana akazi a Tselofekadi anena zaona; uwapatse ndithu colowa cikhale cao cao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse colowa ca atate wao.
8. Ndipo unene ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Akafa munthu wamwamuna wopanda mwana wamwamuna, colowa cace acilandire mwana wace wamkazi.
9. Ndipo akapanda kukhala naye mwana wamkazi, mupatse abale ace colowa cace.