4. Ndipo khamu lace, ndi owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri, mphambu zinai, kudza mazana asanu ndi limodzi.
5. Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Isakara; ndipo kalonga wa ana a Isakara ndiye Netandi mwana wa Zuwara.
6. Ndipo khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.