Numeri 19:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo iye wakutentha ng'ombeyo atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

9. Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe ya msotiyo, nawaike kunja kwa cigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a lsrayeli akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yaucimo.

10. Ndipo wakuola mapulusayo a ng'ombe ya msoti atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israyeli, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.

11. Iye wakukhudza mtembo wa munthu ali yense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;

12. iyeyo adziyeretse nao tsiku lacitatu, ndi pa tsiku lacisanu ndi ciwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lacitatu, sadzakhala woyera tsiku lacisanu ndi ciwiri.

13. Ali yense wakukhudza mtembo wa munthu ali yense wakufa, osadziyeretsa, aipsa kacisi wa Yehova; amsadze munthuyo kwa Israyeli; popeza sanamwaza madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwace kukali pa iye.

14. Cilamulo ndi ici: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

Numeri 19