7. Ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe mucite nchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsaru yocinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani nchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.
8. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israyeli; cifukwa ca kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna, likhale lemba losatha.
9. Izi ndi zako pa zinthu zopatulikitsa, zosafika kumoto; zopereka: zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zaucimo, ndi nsembe zao zonse zoparamula, zimene Andibwezera Ine, zikhale zopatulikitsa za iwe ndi za ana ako amuna.