Numeri 18:12-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa, zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe.

13. Zipatso zoyamba zonse ziri m'dziko mwao, zimene amadza nazo kwa Yehova, zikhale zako; oyera onse a m'banja lako adyeko.

14. Ziri zonse zoperekedwa ciperekere m'Israyeli ndi zako.

Numeri 18