7. Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m'cihema ca mboni.
8. Ndipo kunali m'mawa mwace, kuti Mose analowa m'cihema ca mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, nionetsa timaani, nicita maluwa, nipatsa akatungurume.
9. Ndipo Mose anaturutsa ndodo zonse kuzicotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israyeli; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yace.
10. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kulika cakuno ca mboni, isungike ikhale cizindikilo ca pa ana opikisana; kuti unelitsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.
11. Ndipo Mose anacita monga Yehova adamuuza, momwemo anacita.