3. Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkuru yense wa nyumba za makolo ao.
4. Ndipo uziike m'cihema cokomanako, cakuno ca mboni, kumene ndikomana ndi inu.
5. Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israyeli amene adandaula nao pa inu.
6. Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, ndipo akalonga ao onse anapereka, yense ndodo imodzi, monga mwa mabanja a makolo ao, ndodo khumi ndi ziwiri; ndi ndodo ya Aroni inakhala pakati pa ndodo zao.