Numeri 16:37-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. Nena ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, kuti aphule mbale zofukiza pakati pa moto, nutaye makalawo uko kutali; pakuti ziri zopatulika;

38. mbale zofukizazo za iwo amene adacimwira moyo wao wao, ndipo azisule zaphanthiphanthi, zikhale cibvundikilo ca guwa la nsembe; popeza anabwera nazo pamaso pa Yehova, cifukwa cace zikhala zopatulika; ndipo zidzakhala cizindikilo kwa ana a Israyeli.

39. Ndipo Eleazara wansembe anatenga mbale zofukiza zamkuwa, zimene anthu opsererawo adabwera nazo; ndipo anazisula zaphanthiphanthi zikhale cibvundikilo ca guwala nsembe;

40. cikhale cikumbutso kwa ana a Israyeli, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kucita cofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lace; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.

41. Koma m'mawa mwace khamu lonse la ana a Israyeli anadandaula pa Mose ndi Aroni, nati, Mwapha anthu a Yehova, inu.

Numeri 16