41. Ndipo Mose anati, Mutero cifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako?
42. Musakwereko, pakuti Yehova sali pakati pa inu; kuti angakukantheni adani anu.
43. Pakuti Aamaleki ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, cifukwa cace Yehova sadzakhala nanu.
44. Koma anakwera pamwamba pa phiri modzikuza; koma likasa la cipangano la Yehova, ndi Mose, sanacoka kucigono.
45. Pamenepo anatsika Aamaleki, ndi Akanani, akukhala m'phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horima.