Numeri 13:32-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo anaipsira ana a Israyeli mbiri ya dziko adalizonda, nati, Dzikoli tapitamo kulizonda, ndilo dziko lakutheramo anthu okhalamo; ndi anthu onse tidaona pakati pace ndiwo anthu atali misinkhu.

33. Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati zinsidzi; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.

Numeri 13