Numeri 13:2-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndirikupatsa ana a Israyeli; utumize munthu mmodzi wa pfuko liri lonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzace.

3. Ndipo Mose anawatumiza kucokera ku cipululu ca Parana monga mwa mau a Yehova; amuna onsewa ndiwo akuru a ana a Israyeli.

4. Maina ao ndi awa: wa pfuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri.

5. Wa pfuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori.

6. Wa pfuko la Yuda, Kalebi mwana wa Yefune.

7. Wa pfuko la Isakara, Igali mwana wa Yosefe.

8. Wa pfuko la Efraimu, Hoseya mwana wa Nuni.

9. Wa pfuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu.

10. Wa pfuko la Zebuloni, Gadiyeli mwana wa Sodi.

11. Wa pfuko la Yosefe, wa pfuko la Manase, Gadi mwana wa Susi.

12. Wa pfuko la Dani, Amiyeli mwana wa Gemali.

13. Wa pfuko la Aseri, Setri mwana wa Mikayeli.

14. Wa pfuko la Nafitali, Nabi mwana wa Vopisi.

15. Wa pfuko la Gadi, Geyuelimwana wa Maki.

16. Awandi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamucha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.

17. Potero Mose anawatuma azonde dziko la Kanani, nanena nao, Kwerani uko kumwela, nimukwere kumapiri;

18. mukaone dziko umo liriri; ndi anthu akukhala m'mwemo, ngati ali amphamvu kapena ofok a, ngati acepa kapena acuruka;

19. ndi umo liriri dzikoli lokhalamo iwo, ngati lokoma, kapena loipa; ndi umo iriri midziyo akhalamo iwo, ngati akhala poyera kapena m'malinga;

20. ndi umo iriri nthaka, ngati yopatsa, kapena yosuka, ngati pali mitengo, kapena palibe, Ndipo limbikani mtima, nimubwere nazo zipatso za m'dzikomo. Koma nyengoyi ndiyo nyengo yoyamba kupsa mphesa.

Numeri 13