12. Asakhaletu iye ngati wakufa, amene dera lina la mnofu wace watha poturuka iye m'mimba mwa mace.
13. Ndipo Mose anapfuulira kwa Yehova, ndi kuti, Mciritsenitu, Mulungu,
14. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wace akadamlabvulira malobvu pankhope pace sakadacita manyazi masiku asanu ndi awiri? ambindikiritse kunja kwa cigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.