Numeri 10:3-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la cihema cokomanako,

4. Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akuru a zikwi a m'Israyeli, azisonkhana kuli iwe.

5. Mukaliza cokweza, ayende a m'zigono za kum'mawa.

6. Mukalizanso cokweza, a m'zigono za kumwela ayende; alize cokweza pakumuka.

Numeri 10