Nehemiya 8:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodayi, Maaseya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu cilamuloco; ndi anthu anali ciriri pamalo pao,

8. Nawerenga iwo m'buku m'cilamulo ca Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa cowerengedwaco.

9. Ndipo Nehemiya, ndiye kazembe, ndi Ezara wansembe mlembiyo, ndi Alevi ophunzitsa anthu, ananena ndi anthu onse, Lero ndilo lopatulikira Yehova Mulungu wanu, musamacita maliro, musamalira misozi. Popeza anthu onse analira misozi pakumva mau a cilamulo.

10. Nanena naonso, Mukani mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lace iye amene sanamkonze ratu kanthu; cifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamacita cisoni; pakuti cimwemwe ca Yehova ndico mphamvu yanu.

11. Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli cete; pakuti lero ndi lopatulika; musamacita cisoni.

Nehemiya 8