4. Mudziwo tsono ndi wacitando, ndi waukuru; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.
5. Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufuru, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa cibadwidwe cao. Ndipo ndinapeza buku la cibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo.
6. Ana a dziko amene anakwera kucokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babulo adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense ku mudzi wace, ndi awa:
7. ndiwo amene anadza ndi Zerubabele: Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Moredekai, Bilisani, Misiperete, Bigivai, Nehumu, Baana. Mawerengedwe a amuna a anthu Aisrayeli ndiwo:
8. ana a Parosi zikwi ziwiri mphambu zana limodzi kudza makumi asanu ndi awiri.