Nehemiya 7:15-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ana a Binui, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu.

16. Ana a Betai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

17. Ana a Azigadi, zikwi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi awiri ndi awiri.

18. Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi, kudza asanu ndi awiri.

19. Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi awiri.

20. Ana a Adini, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu.

21. Ana a Aberi, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi atatu.

22. Ana a Hasumu, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

23. Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza anai.

24. Ana a Harifi, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.

Nehemiya 7