Nehemiya 7:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oyimbira, ndi Alevi;

2. ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.

3. Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala m'Yerusalemu, yense polindirira pace, yense pandunji pa nyumba yace.

4. Mudziwo tsono ndi wacitando, ndi waukuru; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.

Nehemiya 7