Nehemiya 6:18-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti ambiri m'Yuda analumbirirana naye cibwenzi; popeza ndiye mkamwini wace wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wace Yehohanana adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.

19. Anachulanso nchito zace zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza akalata kuti andiopse ine.

Nehemiya 6