16. Ndipo kunali atacimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti nchitoyi inacitika ndi Mulungu wathu.
17. Masikuwo aufulu a Yuda analemberanso akalata ambiri kwa Tobiya; ndipo anawafikanso akalata ace a Tobiya.
18. Pakuti ambiri m'Yuda analumbirirana naye cibwenzi; popeza ndiye mkamwini wace wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wace Yehohanana adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.
19. Anachulanso nchito zace zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza akalata kuti andiopse ine.