10. Pamenepo ndinalowa m'nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane ku nyumba ya Mulungu m'kati mwa Kacisi, titsekenso pa makomo a Kacisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe.
11. Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? ndani wonga ine adzalowa m'Kacisi kupulumutsa moyo wace? sindidzalowamo.
12. Ndipo ndinazindikira kuti sanamtuma Mulungu; koma ananena coneneraco pa ine, popeza Tobiya ndi Sanibalati adamlembera.