18. Alevi onse m'mudzi wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai.
19. Ndi odikira: Akubu, Talimoni, ndi abale ao akulindira pazipata, ndiwo zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.
20. Ndi Aisrayeli otsala, ndiwo ansembe ndi Alevi, anakhala m'midzi yonse ya Yuda, yense m'colowa cace.
21. Koma Anetini anakhala m'Ofeli, ndi Ziya, ndi Gisipa anali oyang'anira Anetini.