1. Pali coipa ndaciona kunja kuno cifalikira mwa anthu,
2. munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa cuma ndi ulemu, mtima wace susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ici ndi cabe ndi nthenda yoipa,
3. Cinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zace ndi kucuruka, koma mtima wace osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;