9. Phindutu la dziko lipindulira onse; ngakhale mfumu munda umthandiza.
10. Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda cuma sadzakhuta phindu; icinso ndi cabe.
11. Pocuruka katundu, akudyapo acurukanso; nanga apindulira eni ace ciani, koma kungopenyera ndi maso ao?
12. Tulo ta munthu wogwira nchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.
13. Pali coipa cobvuta ndaciona kunja kuno, ndico, cuma cirikupweteka eni ace pocikundika;
14. koma cumaco cionongeka pomgwera tsoka; ndipo akabala mwana, m'dzanja lace mulibe kanthu.
15. Monga anaturuka m'mimba ya amace, adzabweranso kupita wamarisece, monga anadza osatenga kanthu pa nchito zace, kakunyamula m'dzanja lace.