Mlaliki 3:11-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Cinthu ciri conse anacikongoletsa pa mphindi yace; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse nchito Mulungu wazipanga ciyambire mpaka citsiriziro.

12. Ndidziwa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kucita zabwino pokhala ndi moyo.

13. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m'nchito zace zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.

Mlaliki 3